UNDUNA WA ZAUMOYO CHIDZIWITSO- CHITSIMIKIZO CHA KUPITILILA KUPELEKA THANDIZO LOLIMBANA NDI KACHILOMBO KA HIV NDI MATENDA A EDZI MUZIPATALA ZONSE ZA DZIKO LINO

Unduna wa zaUmoyo ukudziwitsa anthu kuti ntchito yopeleka thandizo lolimbana ndi kachilombo ka HIV lipitilila muzipatala zonse za dziko lino .
Undunawu ukudziwitsa anthu kuti tili ndi mankhwala a ARV ndi mankhwala ena onse olimbana ndi kachilombo ka HIV ndi matenda a Edzi okwanila m’dziko muno. Kuonjezera apo, undunawu ukuyembekezera kulandilaso mankhwala ena ndipo upitilila kudziwitsa anthu za mmene mankhwalawa azibwelela m’dziko muno.


Undunawu ukulangiza anthu kuti asade nkhawa popeza uchilimika kugwila ntchito usana ndi usiku kuonetsetsa kuti mankhwala akupezeka okwanira mu nzipatala zonse za dziko lino. Adindo onse oyang’anila ntchito za umoyo m’dziko muno alangizidwa kuti achilimike ndipo ali okonzeka kuonetsetsa kuti ntchito za umoyo zipitilile kukhala m’nchimake.


Dr. Samson Mndolo
MLEMBI MU UNDUNA WA ZAUMOYO
29th January, 2025

Leave a Reply

Your email address will not be published.