KUCHULUKA KWA NCHITIDWE OFALITSA MAUTHENGA ABODZA OKHUDZA MANKHWALA A HIV NDI EDZI MMASAMBA A MCHEZO

Mabungwe a National AIDS Commission (NAC) ndi Pharmacy and Medicines Regulatory Authority (PMRA) adapatsidwa mphamvu ndi malamulo yowunika ndi kuvomereza mauthenga okhudza matenda a edzi komanso kuwonetsetsa kuti mankhwala achipatala, mankhwala a zitsamba ndi zakudya kapena zakumwa zimene zili mgulu la mankhwala ndi zabwino, zotetezeka ndi zogwira ntchito bwino, komanso kuti malamulo okhudza ntchito za mankhwala akutsatidwa.

Mabungwewa ndi okhumudwa ndi kufala kwa mchitidiwe omwe anthu ena akuchita pomafalitsa mauthenga abodza okhudza matenda a edzi kudzera mmasamba a mchezo monga TikTok, Facebook komanso WhatsApp.

Kafukufuku wa posachedwa yemwe mabungwe a NAC ndi PMRA mogwirizana ndi nthambi ya Polisi achita, wapeza kuti pali akamberembere ena omwe akumagula mankhwala odziwika mma pharmacy, kumatula/kuchotsa zolembedwa pa mankhwalawo ndi kumata ma sitika olemba kuti Gammora, kenaka nkuyamba kutsatsa mankwalawo nkumawauza anthu kuti ndi katemera wa mankhwala omwe amapheratu HIV. Mankhwala achinyengowa akumawagulitsa pa mtengo wapakati pa K90,000 ndi K260,000. Dziwani kuti mauthenga achinyengowa ali ndi kuthekera koika miyoyo ya anthu ochuluka omwe ali ndi HIV pa chiopsezo.

Pa 13 March chaka chino, bwalo la Majesitileti ku Mangochi lidapeza amayi awiri olakwa ndi kuwalipilitsa chindapusa cha ndalama zokwana pafupifipi 2.5 miliyoni kwacha aliyense pa mlandu ogulitsa mankhwala a jakiseni a gentamicin omwe amati ndi katemera wa Gammora yemwe amapheratu HIV. Amayiwa amagula gentamicin-yo ku Pharmacy, kufufuta malemba, kenaka ndi kumata mawu olemba kuti Gammora vaccine yemwe amagulitsa kwa anthu omwe ali ndi HIV pa mtengo wa pakati pa K90,000 ndi K120,000 pa mulingo wa timabotolo titatu.

Ndipo Pa 13 June chaka chomwe chino, bwalo la Majesitileti ku Mwanza lidalamula bambo wina wa zaka 32 kukakhala ku ndende kwa miyezi khumi ndi isanu (15) pa mlandu ogulitsa mankhwala amapilisi osadziwika omwenso amati ndi Gammora ochiza HIV.  Mlandu wina ukupitilira ku bwalo la Majesitileti ku Zomba komwe mnyamata wina yemwe ndi ophunzira pa sukulu ya ukachenjede ya University of Malawi akuyankha mlandu ngati omwewu.

Mabungwe a NAC ndi PMRA akukumbutsa anthu onse kuti pakadali pano mankhwala a HIV sadapezekebe. Mankhwala omwe alipo ndi aja ama ARV omwe amathandiza kuti HIV isachulukane mthupi mwa munthu yemwe alinayo. Dziwani kuti kumwa ma ARV mwandondomeko kumachepetsa chiwerengero cha HIV kufika pa mulingo wakuti nthawi zina osapezekaso pamene munthu wapita kukayezetsa HIV yi kuchipatala. Anthu ena akumatenga zotsatira zoterezi ngati umboni wosonyeza kuti munthu wachila ku HIV pambuyo pakugwiritsa ntchito mankhwala achinyengowa a Gammora.

Anthu, makamaka omwe ali pa ma ARV akuchenjezedwa kuti asanamizidwe kuti kutsika kwa chiwerengero kapenanso kusapezeka kumene kwa HIV mthupi mwawo ndi kamba ka mankhwala achinyengowa; ndi ma ARV okha omwe amatsitsa chiwerengero cha HIV zomwe zimathandizira kuti munthu akhale ndimoyo wathanzi komanso kuti asapatsire ena.

Mabungwe awiriwa akupempha anthu omwe ali ndi HIV kuti akhale ochilimika ndikuonetsetsa kuti akumafunsa uphungu wachipatala nthawi zonse kuti alandire mankhwala oyenera komanso kupatsidwa malangizo akagwiritsidwe ntchito ka mankhwala kotetezeka. Kumwa mankhwala mosatsatira uphungu wachipatala kumadzetsa mavuto osiyanasiyana monga kugwiritsa ntchito mankhwala osagwirizana ndi matenda omwe munthu ali nawo.

Pambali pakuti mchitidwe wogulitsa mankhwala achinyengowa ukuika miyoyo ya anthu pachiopsezo, mchitidwewu ukusokonezanso ntchito yabwino yomwe achipatala komanso mabungwe a boma akugwira yoteteza umoyo wa a Malawi poonetsetsa kuti mankhwala omwe akupezeka mdziko muno ndi abwino, otetezeka ndi ogwira ntchito bwino. Awa ndi ena mwa mavuto omwe abwera chifukwa cha mchitidwe wogulitsa mankhwala achinyengowa:

  1. Anthu akupatsidwa mankhwala osagwirizana ndi matenda awo zomwe zitha kudzetsa mavuto osaneneka kuphatikizapo imfa;
  • Anthu omwe ali pa mankhwala ama ARV akusiyira mankhwala panjira pomaganiza kuti apeza mankhwala ena omwe ali ndi kuthekera kopheratu HIV. Izi zitha kubweretsa mtundu wa HIV osamva mankhwala zomwe mapeto ake ndi kuluza miyoyo;
  • Mankhwala ogulitsidwa mwa chinyengowa akumatha mphamvu nthawi yawo isanakwane chifukwa chakuti akumasungidwa malo osayenera kusunga mankhwala. Dziwani kuti mankhwala omwe atha mphamvu amatha kusanduka poizoni yemwe akhoza kudzetsa matenda ena oopsa kapenanso imfa;
  • Komanso pozindikila kuti HIV imadzetsa kusalana, anthu omwe akumagula Gammora obaya akumazibaya okha majakiseni kapena kuuza ena omwe alibe ukadaulo wa chipatala kuti awabaye poopa kuti angadziwike kuti ali ndi HIV. Izi zili ndikuthekera kobweretsa mavuto monga kufa kwa ziwalo kamba kozibaya mitsempha yolakwika. Kuonjezera apo, palinso chiopsezo chakupitirira kufala kwa HIV kamba kakuti majakiseni omwe anthuwa agwiritsa kale ntchito amatayidwa paliponse posatsata ndondomeko yoyenera.

Choncho mabungwe a NAC ndi PMRA akuchenjeza anthu onse kuti kufalitsa uthenga wabodza okhudza HIV ndi Edzi  ndi mulandu malinga ndi Gawo 25 la malamulo a Bungwe la NAC. Komanso, malinga ndi Gawo 98 la malamulo a Bungwe la PMRA, aliyense opezeka akupanga, kuitanitsa kuchokera kunja, kapena kugulitsa mankhwala achinyengo akupalamula mulandu.

Mabungwewa apitirira kugwira ntchito ndi nthambi zina za boma monga Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) komanso a Polisi ndi cholinga chakuti milandu yonse yokhudza kugulitsa mankhwala abodza ochiza HIV kuphatikizapo a Gammora ifufuzidwe ndipo onse omwe akuchita izi agwide ndi kuzengedwa mlandu. Aliyense yemwe akudziwa omwe akupanga mchitidwewu kapena mchitidwe uliwonse ogulitsa mankhwala mwachinyengo atsine khutu ma bungwe a NAC ndi PMRA kapena akanene ku Polisi.

Mukafuna kumva zambiri pa nkhaniyi, funsani mkulu wofalitsa nkhani ku Bungwe la PMRA pa 0885 313 011 kapena kutumiza email pa jjosiah@pmra.mw. Muthanso kuyankhula ndi wogwirizira udindo wa mkulu wofalitsa nkhani ku Bungwe la NAC pa 0999 331 716 kapena kutumiza email pa mabedif@aidsmalawi.org.mw.

Leave a Reply

Your email address will not be published.