WOFALITSA ZABODZA ZOKHUDZANA MACHIRITSO A HIV AWERUZIDWA KUTI AKHALE M’NDENDE MIYEZI KHUMI NDI MPHAMBU ZISANU (15)

WOFALITSA ZABODZA ZOKHUDZANA MACHIRITSO A HIV AWERUZIDWA KUTI AKHALE M’NDENDE MIYEZI KHUMI NDI MPHAMBU ZISANU (15)

Bwalo la milandu laling’ono ku Mwanza lalamula a Petros Jasi kukakhala mu ndende chifukwa chonamiza anthu kuti ali ndi mankhwala omwe amachiza HIV dzina lake  ‘Gamora wochiza HIV’.                                                                                                  

Masamba a Intaneti a mchezo adzadza ndi zonena za anthu ena omwe akumati ali ndi mankhwala omwe amachiza HIV omwe amatchedwa ‘Gamora wochiza HIV’.

Anthuwa akhala akufalitsa nkhani yabodzayi potsatsa mankhwala osatsimikizikawa pogwiritsa ntchito masamba a mchezo a WhatsApp ndi Facebook.

Anthu amenewa amayesetsa kuti asakumane maso ndo maso ndi ma kasitomala awo. Amalandira ndalamazo kudzera ku njira yolandilira ndalama mu foni zam’manja ndipo nthawi zambiri amatumiza mankhwala abodzawa kwa omwe amawagulawo popanda kukumana nawo, kuti asadziwike.

Sichapafupi kuwapeza anthuwa komanso kudziwa komwe akupezeka chifukwa amagwiritsa ntchito ma nambala a foni omwe analembetsedwa m’mayina a nzika zina za dziko lino popanda eni akewo kudziwa za ichi.

Pochita izi, makasitomala ena osalakwa omwe ali ndi HIV akuberedwa ndalama ndi kunamizidwa kuti alandira chithandizo choyenera. Anthu ena omwe ali ndi HIV amakhulupirira kuti mankhwalawa ndi machiritso ndipo amasiya kumwa mankhwala ochepetsa mphamvu ya HIV a ma ARV.

M’mwezi wa May 2024, mabungwe a National AIDS Commission (NAC), Pharmacy and Medicines Regulatory Authority (PMRA), ndi Malawi Police Service (MPS) anayambanso kugwira ntchito yofufuza anthu omwe amafalitsa nkhani zabodza m’masamba a mchezo kuti ali ndi mankhwala ochizira HIV. Pa 31 May 2024, a Polisi anagwira bambo Petros Jasi pa Zalewa Road Block pamene ankafuna kugulitsa mankhwala otchedwa “Gamora wochiza HIV”  kwa kasitomala.

Mkuluyu adamutengera ku bwalo lamilandu la m’boma la Mwanza komwe  anamuzenga mlandu wophwanya lamulo lokhazikitsa ndondomeko za kapewedwe ndi ntchito zolimbana ndi HIV ndi Edzi la 2018 komanso anaphwanya lamulo la Poisons and Medicines Regulatory Authority (PMRA) la 2019.

Bwaloli linapeza oganiziridwayo ndi mlandu wofalitsa uthenga osocheretsa, komanso wabodza wokhudza machiritso a HIV malingana ndi ndime 25 ya lamulo lokhazikitsa ndondomeko za kapewedwe ndi ntchito zolimbana ndi HIV ndi Edzi la 2018. Oganiziridwayo adapezekanso ndi mlandu wotsatsa mankhwala popanda chilolezo malinga ndi gawo 68 la Poisons and Medicines Regulatory Authority (PMRA) Act la 2019. Pamapeto pake adapezeka wolakwa pamilandu yonse iwiri.

Oyimira boma pa mlanduwu adapempha bwalo kuti mkuluyi apatsidwe chilango chokhwima poganizira kuti mlanduwu wapangitsa kuti anthu ena omwe ali ndi HIV asiye kumwa ma ARV zomwe zingapangitse kuti miyoyo yawo iwonongeke kapena kuti thanzi lichepe pamiyoyo yawo kamba kosatsatira ndondomeko ya kamwedwe ka ma ARV.

Popereka chigamulo, oweluza mlandu adagwirizana ndi oyimira boma pa mlanduwu kuti kuchuluka kwa nkhani zabodzazi kuli ndi zotsatira zoyipa zomwe zitha kuwononga momwe  ntchito yolimbana ndi HIV mdziko muno ikuyendera. Pa chifukwa ichi, woganiziridwayo adagamulidwa kuti akakhale ku ndende miyezi khumi ndi mphambu zisanu (15) ndipo analibe mwai olipila chindapusa.

Chigamulochi chikupeleka chenjezo kwa onse amene akudyera masuku pamutu ena amene ali pachiopsezo cha HIV pofalitsa nkhani zabodza. Anthu akulimbikitsidwa kukhala osamala ndi kufunafuna zidziŵitso zolondola kuchokera ku malo odalirika. Bungwe la NAC likukumbutsanso anthu kuti kumwa ma ARV ndinjira yokhayo yovomerezeka yochepetsera mphamvu ya HIV mthupi ndi kulimbitsa Thanzi kwa amene ali ndi HIV.

M’mbuyomu, m’mwezi wa March 2024, bwalo la milandu m’boma la Mangochi linapereka chindapusa kwa amayi awiri kuti alipire ndalama zokwana K2.5 miliyoni aliyense chifukwa chogulitsa mankhwala a jekeseni wa gentamicin zomwe zinalembedwa kuti “Gamora jekeseni wochiza HIV”.

NAC, PMRA ndi a Police  ali pamkalikiliki kufunafuna kuti apeze anthu ena omwe akutsatsa ndi kugulitsaa mankhwala abodzawa, omwe atsala.   

A Petros Jasi ndi a zaka 32, ndipo amachokera m’mudzi wa Tulonkhondo mwa Mfumu yaikulu Kanduku m’boma la Mwanza.

Leave a Reply

Your email address will not be published.